7 Simunaona masomphenya opanda pace kodi? simunanena ula wabodza kodi? pakunena inu, Atero Yehova; cinkana sindinanena?
8 Cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Popeza mwanena zopanda pace, ndi kuona mabodza, cifukwa cace taonani, ndikhala Ine wotsutsana nanu, ati Ambuye Yehova.
9 Ndi dzanja langa lidzakhala lotsutsana nao aneneri akuona zopanda pace, ndi kupenda za bodza; sadzakhala mu msonkhano wa anthu anga, kapena kulembedwa m'buku lolembedwamo nyumba ya Israyeli, kapena kulowa m'dziko la Israyeli; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Yehova,
10 Popeza, inde popeza asokeretsa anthu anga, ndi kuti, Mtendere, pokhala palibe mtendere; ndipo anthu akamanga linga, aneneriwo alimata ndi dothi losapondeka;
11 uziti nao olimata ndi dothi losapondeka, kuti lidzagwa, lidzabvumbidwa ndi mvula yaikuru; ndi inu, matalala akuru, mudzagwa; ndi mkuntho udzalithithimula.
12 Ndipo taonani, litagwa linga, sadzanena nanu kodi, Liri kuti dothi munalimata nalo?
13 Cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Ndidzalithithimula ndi mkuntho m'ukali wanga; ndipo lidzabvumbidwa ndi mvula yaikuru mu mkwiyo wanga, ndi matalala akuru adzalitha m'ukali wanga.