15 Koma unatama kukongola kwako, ndi kucita zacigololo potama mbiri yako, ndi kutsanulira zigololo zako pa munthu ali yense wopitapo; unali wace.
16 Ndipo unatengako zobvala zako, ndi kudzimangira misanje ya mawanga mawanga, ndi kucitapo cigololo; zotere sizinayenera kufika kapena kucitika.
17 Unatenganso zokometsera zako zokoma za golidi wanga ndi siliva wanga, zimene ndinakupatsa, ndi kudzipangira mafano a amuna, ndi kucita nao cigololo.
18 Unatenganso zobvala zako za nsaru yopikapika, ndi kuwabveka nazo, unaikanso mafuta anga ndi cofukiza canga pamaso pao.
19 Ndi mkate wanga ndinakupatsawo, ufa wosalala, ndi mafuta, ndi uci, ndinakudyetsazo, unawaikira izi pamaso pao, zicite pfungo lokoma; kunatero, ati Ambuye Yehova.
20 Unatenganso ana ako amuna ndi akazi amene unandibalirawo, ndi kuwapereka nsembe awathe. Zigololo zako zidacepa kodi,
21 kuti unawapha ana anga ndi kuwapereka, pakuwapititsa pamoto?