34 M'mwemo usiyana konse ndi akazi ena m'cigololo cako; pakuti palibe wokutsata kucita nawe cigololo; popezanso uwalipira, koma sakupatsa iwe mphotho; potero usiyana nao konse ena.
35 Cifukwa cace, wacigololo iwe, tamvera mau a Yehova:
36 Atero Ambuye Yehova, Popeza ndalama zako zamwazika, nubvundukuka umarisece wako mwa cigololo cako ndi mabwenzi ako, ndi cifukwa ca mafano onse a zonyansa zako, ndi mwazi wa ana ako umene unawa patsa;
37 cifukwa cace taona, ndidzasonkhanitsa mabwenzi ako onse amene wakondwera nao, ndi onse unawakonda, pamodzi ndi onse unawada; inde ndidzawasonkhanitsira iwe pozungulira ponse, ndi kuwabvundukulira umarisece wako, kuti aone umarisece wako wonse.
38 Ndipo ndidzaweruza mlandu wako, monga aweruza akazi acigololo ndi okhetsa mwazi; ndipo ndidzakutengera mwazi wa ukali ndi wa nsanje.
39 Ndidzakuperekanso m'dzanja lao, ndipo adzagwetsa nyumba yako yacimphuli, ndi kugumula ziunda zako, nadzakubvula zobvala zako, ndi kulanda zokometsera zako zokongola, nadzakusiya wamarisece ndi wausiwa.
40 Ndipo adzamemezera iwe msonkhano, nadzakuponya miyala, ndi kukupyoza ndi malupanga ao.