4 Ndipo za kubadwa kwako, tsiku lobadwa iwe sanadula ncofu yako, sanakuyeretsa ndi kukusambitsa ndi madzi, sanakuthira mcere konse, kapena kukukulunga m'nsaru ai.
5 Panalibe diso linakucitira cifundo, kukucitira cimodzi conse ca izi, kucitira iwe nsoni; koma unatayidwa kuyere; pakuti ananyansidwa nao moyo wako tsiku la kubadwa kwake,
6 Ndipo popita Ine panali iwepo, ndinakuona ulikubvimvinizika m'mwazi wako. Pamenepo ndinanena ndi iwe m'mwazi wako, Khala ndi moyo, inde ndinati kwa iwe m'mwazi mwako, Khala ndi moyo.
7 Ndinakucurukitsa ngati mphundu za kumunda; ndipo unathululuka ndi kukula kufikira wakongola nkhope, maere ako anamera, ndi tsitsi lako linamera; koma unali wamarisece ndi wausiwa.
8 Ndipo popita Ine panali iwepo ndi kukupenya, taona nyengo yako ndiyo nyengo yakukondana; pamenepo ndinakupfunda copfunda canga, ndi kuphimba umarisece wako; inde ndinakulumbirira ndi kupangana nawe, ati Ambuye Yehova, ndipo unakhala wanga.
9 Ndipo ndinakusambitsa ndi madzi, inde ndinakutsuka kukucotsera mwazi wako, ndi kukudzoza mafuta.
10 Ndinakubvekanso ndi nsaru zopikapika, ndi kukubveka nsapato za cikopa ca katumbu; ndinakuzenenga nsaru yabafuta, ndi kukuphimba ndi nsaru yasilika.