1 Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti,
2 Wobadwa ndi munthu iwe, ipha mwambi, nunene fanizo kwa nyumba ya Israyeli,
3 nuziti, Atero Ambuye Yehova, Ciombankhanga cacikuru ndi mapiko akuru, ndi maphiphi atali, odzala nthenga ca mathotho-mathotho, cinafika ku Lebano, nicitenga nsonga ya mkungudza,
4 cinabudula nsonga yosomphoka ya nthambi zace zanthete, ndi kumuka nayo ku dziko la malonda, cinaiika m'mudzi wa amalonda.
5 Cinatengakonso mbeu ya m'dziko, ndi kuibzala m'nthaka yokoma, cinaiika panali madzi ambiri, cinaioka ngati mtengo wamsondodzi.
6 Ndipo inaphuka, nikhala mpesa wotambalala wofupi msinkhu, nthambi zace zinapindikira momwe, ndi mizu yace pansi pace, nikhala mpesa, nuonetsa nthambi ndi kuphuka mphukira.