7 Panalinso ciombankhanga cina cacikuru, ndi mapiko akuru, ndi nthenga zambiri; ndipo taona, mpesa uwu unacipindira mizu yace, nucilunjikitsira nthambi zace, kucokera pookedwa pace, kuti ciuthirire madzi.
8 Unaokedwa mu nthaka yabwino kuli madzi ambiri, kuti uphuke nthambi, nubale zipatso, nukhale mpesa wabwino.
9 Uziti, Atero Ambuye Yehova, Udzakondwa kodi? sadzausula ndi kudula zipatso zace, kuti uume, kuti masamba ace onse ophuka aume, ngakhale palibe mphamvu yaikuru, kapena anthu ambiri akuuzula?
10 Inde ungakhale waokedwa udzakondwa kodi? sudzauma ciumire kodi pakuuomba mphepo ya kum'mawa? udzauma pookedwa apo udaphuka.
11 Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti.
12 Uziti tsono kwa nyumba ya mpandukoyi, Simudziwa kodi izi nciani? Uziti, Taonani mfumu ya ku Babulo inadza ku Yerusalemu, nitenga mfumu yace ndi akalonga ace, nibwera nao kuti iye ku Babulo;
13 nitenga wa mbumba yacifumu, nicita naye pangano, nimlumbiritsa, nicotsa amphamvu a m'dziko;