24 Koma wolungamayo akabwerera kuleka cilungamo cace, nakacita mphulupulu, ndi kucita monga mwa zonyansa zonse azicita woipa, adzakhala ndi moyo kodi? Nnena cimodzi ca zolungama zace zonse adzazicita cidzakumbukika m'kulakwa kwace analakwa nako, ndi m'kucimwa kwace anacimwa nako; momwemo adzafa.
25 Koma mukuti, Njira ya Ambuye njosayenera. Tamvera tsono nyumba ya Israyeli, Kodi njira yanga njosayenera? njira zanu si ndizo zosayenera?
26 Wolungamayo akatembenukira kuleka cilungamo cace, nakacita mphulupulu, adzafa momwemo; m'mphulupulu yace adaicita adzafa.
27 Ndipo woipayo akatembenukira kuleka coipa cace adacicita, nakacita ciweruzo ndi cilungamo, adzapulumutsa moyo wace.
28 Popeza anasamalira, natembenukira kuleka zolakwa zace zonse adazicita, adzakhala ndi moyo ndithu, sadzafa.
29 Koma nyumba ya Israyeli imanena, Njira ya Ambuye njosayenera, Inu, nyumba ya Israyeli, kodi njira zanga nzosayenera? njira zanu si ndizo zosayenera?
30 Cifukwa cace ndidzakuweruzani inu, nyumba ya Israyeli, yense monga mwa njira zace, ati Ambuye Yehova. Bwererani, nimutembenukire kuleka zolakwa zanu zonse, ndipo simudzakhumudwa nazo, ndi kuonongeka nayo mphulupulu.