4 Waparamula nao mwazi wako, waukhetsa, nudetsedwa nao mafano ako udawapanga, nuyandikizitsa masiku ako, wafikiranso zako zako; cifukwa cace ndakuika ukhale citonzo ca amitundu ndi coseketsa ca maiko onse.
5 Okhala pafupi ndi okhala patali adzakuseka pwepwete, wodetsedwa dzina iwe, wodzala ndi kusokosera.
6 Taona akalonga a Israyeli, yense monga mwa mphamvu yace, akhala mwa iwe, kuti akhetse mwazi.
7 Mwa iwe anapepula atate ndi mai, pakati pa iwe anamcitira mlendo momzunza, mwa iwe anazunza ana amasiye, ndi mkazi wamasiye.
8 Wanyoza zopatulika zanga, waipsa masabata anga.
9 Anthu oneneza anali mwa iwe, kuti akhetse mwazi; ndipo anadya pamapiri mwa iwe, pakati pa iwe anacita zamanyazi.
10 Anabvula umarisece wa atate ao mwa iwe, mwa iwe anacepsa wodetsedwa ndi kooloka kwace.