12 Anaumirira Aasuri, ziwanga, ndi akazembe oyandikizana naye, obvala zangwiro, anthu oyenda pa akavalo, onsewo anyamata ofunika.
13 Ndipo ndinamuona kuti anadetsedwa, onse awiri adatenga njira yomweyi.
14 Ndipo anaonjeza zigololo zace, naona amuna olembedwa pakhoma, zithunzithunzi za Akasidi olembedwa ndi kundwe;
15 omangira malamba m'cuuno mwao, ndi nduwira zazikuru zonika pamitu pao, maonekedwe ao ngati akalonga onsewo, akunga a ku Babulo, dziko la kubadwa kwao ndi Kasidi.
16 Ndipo pakuwaona anawalakalaka, nawatumira mithenga ku dziko la Akasidi.
17 Namdzera a ku Babulo ku kama wa cikondi, namdetsa ndi cigololo cao, iyenso anadetsedwa nao; atatero moyo wace unafukidwa nao.
18 M'mwemo iye anaulula cigololo cace, nabvula umarisece wace; pamenepo moyo wanga unaipidwa naye, monga umo moyo unaipidwira mkuru wace.