1 Anandidzeranso mau a Yehova caka cacisanu ndi cinai, mwezi wakhumi, tsiku lakhumi la mwezi, ndi kuti,
2 Wobadwa ndi munthu iwe, Udzilembere dzina la tsiku lomwe lino, mfumu ya ku Babulo wayandikira Yerusalemu tsiku lomwe lino.
3 Ndipo uphere nyumba yopandukayo fanizo, nunene nao, Atero Ambuye Yehova, Tereka mphika; uutereke, nuthire madzi m'menemo.
4 Longamo pamodzi ziwalo zace, ziwalo zonse zokoma, mwendo wathako ndi wamwamba; uudzaze ndi mafupa osankhika.
5 Tengako coweta cosankhika, nuikire mafupa mulu wa nkhuni pansi; ubwadamuke, ndi mafupa ace omwe uwaphike m'mwemo.