25 Zombo za ku Tarisi ndizo amtengatenga a malonda ako; ndipo unadzazidwa ndi cuma ndi ulemu waukuru pakati pa nyanja,
26 Opalasa ako anakufikitsa ku madzi akuru; mphepo ya kum'mawa inakutyola m'kati mwa nyanja,
27 Cuma cako, zako zogulana nazo malonda ako, amarinyero ako, ndi oongolera ako, amisiri ako, ndi ogulitsa malonda ako, ndi ankhondo ako onse okhala mwa iwe, pamodzi ndi msonkhano wonse uli pakati pa iwe, adzagwa m'kati mwa nyanja tsiku la kugwa kwako.
28 Pakumveka mpfuu wa oongolera ako mabwalo ako adzagwedezeka.
29 Ndi onse ogwira nkhafi, amarinyero, ndi oongolera onse a kunyanja, adzatsika ku zombo zao, nadzaima pamtunda,
30 nadzamveketsa mau ao pa iwe, nadzalira mowawa mtima, nadzathira pfumbi pamitu pao, nadzakunkhulira m'maphulusa,
31 nadzameta mpala, cifukwa ca iwe, nadzadzimangira ziguduli m'cuuno, nadzakulirira ndi mtima wowawa maliro owawa.