4 Ndi lupanga lidzadzera Aigupto, ndi m'Kusi mudzakhala kuwawa kwakukuru, pakugwa ophedwa m'Aigupto; ndipo adzacotsa aunyinji ace, ndi maziko ace adzagadamuka,
5 Kusi, ndi Puti, ndi Ludi, ndi osokonezeka onse, ndi Kubi, ndi anthu a dziko lopangana nao, adzagwa pamodzi nao ndi lupanga.
6 Atero Yehova, Iwonso ocirikiza Aigupto adzagwa, ndi mphamvu yace yodzikuza idzatsika, kuyambira nsanja ya Sevene adzagwa m'kati mwace ndi lupanga, ati Ambuye Yehova.
7 Ndipo adzakhala opasuka pakati pa maiko opasuka, ndi midzi yace idzakhala pakati pa midzi yopasuka.
8 Ndipo adzadziwa, kuti Ine ndine Yehova, nditaika moto m'Aigupto, naonongeka onse akumthandiza.
9 Tsiku ilo mithenga idzaturuka pamaso panga m'zombo kuopsa Akusi osalabadira; ndipo kudzakhala kuwawa kwakukuru pakati pao, monga tsiku la Aigupto, pakuti taona, likudza.
10 Atero Ambuye Yehova, Ndidzaleketsa kusokosera kwa Aigupto ndi dzanja la Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo.