17 Ndipo inu, gulu langa, atero Ambuye Yehova, ndiweruza pakati pa zoweta ndi zoweta, nkhosa zamphongo ndi atonde.
18 Kodi cikuceperani, kuti mwadya podyetsa pabwino? muyenera kodi kupondereza ndi mapazi anu podyera panu potsala? muyenera kumwa madzi ndikha, ndi kubvundulira otsalawo ndi mapazi anu?
19 Ndi nkhosa zanga zidye kodi zoponderezeka ndi mapazi anu, ndi kumwa zobvunduliridwa ndi mapazi anu?
20 Cifukwa cace atero nao Ambuye Yehova, Taonani, Ine, Inedi ndidzaweruza pakati pa zoweta zonenepa, ndi zoweta zoonda.
21 Popeza mukankha ndi nthiti ndi phewa, nimugunda zodwala zonse ndi nyanga zanu, mpaka mwazibalalitsa kubwalo,
22 cifukwa cace ndidzapulumutsa gulu langa lisakhalenso cakudya; ndipo ndidzaweruza pakati pa zoweta ndi zoweta.
23 Ndipo ndidzaziutsira mbusa mmodzi; iye adzazidyetsa, ndiye mtumiki wanga Davide, iye adzazidyetsa, nadzakhala mbusa wao.