23 Ndipo ndidzaziutsira mbusa mmodzi; iye adzazidyetsa, ndiye mtumiki wanga Davide, iye adzazidyetsa, nadzakhala mbusa wao.
24 Ndipo Ine Yehova ndidzakhala Mulungu wao, ndi mtumiki wanga Davide kalonga pakati pao; Ine Yehova ndanena.
25 Ndipo ndidzapangana nazo pangano la mtendere, ndi kuleketsa zirombo zoipa m'dzikomo; ndipo zidzakhala mosatekeseka m'cipululu, ndi kugona kunkhalango.
26 Pakuti ndidzaika izi ndi miraga yozungulira citunda canga; zikhale mdalitso; ndipo ndidzabvumbitsa mibvumbi m'nyengo yace, padzakhala mibvumbi ya madalitso.
27 Ndi mitengo ya kuthengo idzapereka zobala zao, ndi nthaka idzapereka zipatso zace, ndipo adzakhazikika m'dziko mwao; ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, nditadula zomangira goli lao, ndi kuwalanditsa m'manja mwa iwo akuwatumikiritsa.
28 Ndipo sadzakhalanso cakudya ca amitundu, ndi cirombo ca kuthengo sicidzawadyanso; koma adzakhala osatekeseka, opanda wina wakuwaopsa.
29 Ndipo ndidzawautsira mbeu yomveka, ndipo sadzacotsedwanso ndi njala m'dzikomo, kapena kusenzanso manyazi a amitundu.