21 Nunene nao, Atero Ambuye Yehova, Taonani, ndidzatenga ana a Israyeli pakati pa amitundu kumene adamkako, ndi kuwasokolotsa ku mbali zonse, ndi kulowa nao m'dziko mwao;
22 ndipo ndidzawayesa mtundu umodzi m'dzikomo, pa mapiri a Israyeli; ndipo mfumu imodzi idzakhala mfumu ya iwo onse, sadzakhalanso mitundu iwiri, kapena kugawanikanso maufumu awiri konse ai.
23 Ndipo sadzadzidetsanso ndi mafano ao, kapena ndi zonyansa zao, kapena ndi zolakwa zao ziri zonse; koma ndidzawapulumutsa mokhala mwao monse m'mene anacimwamo, ndi kuwayeretsa; m'mwemo adzakhala anthu anga, ndi Ine ndidzakhala Mulungu wao.
24 Ndi mtumiki wanga Davide adzakhala mfumu yao, ndipo iwo onse adzakhala ndi mbusa mmodzi, adzayendanso m'maweruzo anga, nadzasunga malemba anga ndi kuwacita.
25 Ndipo adzakhala m'dziko ndinalipereka kwa Yakobo mtumiki wanga, limene anakhalamo makolo anu, ndipo adzakhala m'mwemo iwo, ndi ana ao, ndi zidzukulu zao kosatha; ndi Davide mtumiki wanga adzakhala mtsogoleri wao kosatha.
26 Ndipo ndidzapangana nao pangano la mtendere, lidzakhala pangano losatha nao, ndipo ndidzawakhazika, ndi kuwacurukitsa, ndi kuika malo anga opatulika pakati pao kosatha.
27 Kacisi wanganso adzakhala nao, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wao, ndi iwo adzakhala anthu anga.