1 Ndipo iwe, wobadwa ndi munthu, nenera motsutsana naye Gogi, uziti, Atero Ambuye Yehova, Taona, nditsutsana nawe Gogi, iwe mfumu yaikuru ya Meseki ndi Tubala;
2 ndipo ndidzakutembenuza, ndi kukutsogolera, ndi kukweza iwe ucoke ku malekezero a kumpoto; ndipo ndidzadza nawe ku mapiri a Israyeli;
3 ndipo ndidzakantha uta wako kuucotsa m'dzanja lako lamanzere, ndi kutayitsa mibvi yako ku dzanja lako lamanja.
4 Udzagwa pa mapiri a Israyeli, iwe ndi magulu ako onse, ndi mitundu ya anthu okhala ndi iwe; ndidzakupereka kwa mbalame zolusa za mitundu yonse, ndi kwa zirombo za kuthengo, akuyese cakudya.
5 Udzagwa kuthengo koyera, pakuti ndanena ndine, ati Ambuye Yehova.
6 Ndipo ndidzatumizira moto Magogi, ndi iwo okhala mosatekeseka m'zisumbu; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
7 Ndipo ndidzadziwikitsa dzina langa loyera pakati pa anthu anga Israyeli, osalola dzina langa loyera aliipsenso; ndipo amitundu adzadziwa kuti Ine ndine Yehova Woyerayo wa Israyeli.