23 Ndipo Kacisi ndi malo opatulikitsa anali nazo zitseko ziwiri.
24 Ndipo pamakomopo panali zitseko zopatukana zotembenuzika, cina copatukana pa khomo lina cina pa linzace.
25 Ndipo panalembedwa pamenepo pa Izitseko za Kacisi akerubi ndi akanjedza, akunga aja adalembedwa pamakhoma; ndipo panali matabwa ocindikira pakhomo pakhonde panja,
26 Ndipo panali mazenera a made okhazikika, ndi akanjedza cakuno ndi cauko, kumbali zace za khonde; momwemonso pa zipinda za m'mphepete mwa nyumba, ndi pa matabwa ocindikira.