14 Atalowa ansembe asaturukenso m'malo opatulika kumka ku bwalo lakunja, koma komweko aziika zobvala zao zimene atumikira nazo; pakuti ziri zopatulika; ndipo abvale zobvala zina, nayandikire zinthu wamba za anthu.
15 Atatha tsono kuyesa nyumba ya m'katimo, anaturuka nane njira ya cipata coloza kum'mawa, nayesa bwalo pozungulira pace.
16 Anayesa mbali ya kum'mawa ndi bango loyesera, mabango mazana asanu, kuyesa ndi bango loyesera, pozungulira pace.
17 Anayesa mbali ya kumpoto mabango mazana asanu, kuyesa ndi bango loyesera, pozungulira pace.
18 Anayesa mbali ya kumwela mabango mazana asanu, kuyesa ndi bango loyesera,
19 Anatembenukira ku mbali ya kumadzulo, nayesa mabango mazana asanu ndi bango loyesera.
20 Analiyesa mbali zace zinai, linali nalo linga pozungulira pace, utali wace mazana asanu, citando cace mazana asanu, kusiyanitsa pakati pa zopatulika ndi zawamba.