10 Wabadwa ndi munthu iwe, onetsa nyumba ya Israyeli kacisiyu, kuti acite manyazi ndi mphulupulu zao; ndipo ayese muyeso wace.
11 Ndipo ngati akacita manyazi nazo zonse anazicita, uwadziwitse maonekedwe a kacisiyu, ndi muyeso wace, ndi poturukira pace, ndi polowera pace, ndi malongosoledwe ace onse, ndi malemba ace onse, ngakhale maonekedwe ace onse, ndi malamulo ace onse; nuwalembere pamaso pao, kuti asunge maonekedwe ace onse, ndi malemba ace onse, nawacite.
12 Lamulo la kacisi ndi ili: pamwamba pa phiri malire ace onse pozungulira pace azikhala opatulikitsa. Taonani, limeneli ndi lamulo la kacisi.
13 Ndipo miyeso ya guwa la nsembe, kuyesa mikono ndi iyi: (mkonowo ndiwo mkono ndi cikhato), tsinde lace likhale mkono, ndi kupingasa kwace mkono, ndi mkuzi wace m'mphepete mwace pozungulira pace kuyesa zala; ili ndi tsinde la guwali.
14 Ndi kuyambira kunsi kwace kunthaka, kufikira phaka lamunsi, mikono iwiri; ndi kupingasa kwace mkono umodzi; ndi kuyambira phaka laling'ono kufikira phaka lalikuru mikono inai; ndi kupingasa kwace mkono.
15 Ndi guwa lapamwamba mikono inai; ndi pamoto pa guwa padzaturuka nyanga zinai.
16 Ndi pamoto pa guwa, m'litali mwace mikono khumi ndi iwiri, ndi kupingasa kwace khumi ndi iwiri, lampwamphwa mbali zace zinai.