19 Upatse ansembe Alevi, a mbeu ya Zadoki, okhala pafupi ndi Ine, kunditumikira Ine, ati Ambuye Yehova, mwana wa ng'ombe, akhale wa nsembe yaucimo.
20 Nutengeko mwazi wace, ndi kupaka pa nyanga zinai za guwa, ndi pa ngondya zinai za phaka, ndi pa mkuzi wace pozungulira; motero uliyeretse ndi kulicitira cotetezera.
21 Utengenso ng'ombe ya nsembe yaucimo, aipsereze pa malo oikika a kacisi kunja kwa malo opatulika.
22 Ndipo tsiku laciwiri upereke tonde wopanda cirema, akhale nsembe yaucimo; ndipo ayeretse guwa la nsembe monga umo analiyeretsera ndi ng'ombeyo.
23 Utatha kuliyeretsa upereke mwana wa ng'ombe wopanda cirema, ndi nkhosa yamphongo ya zoweta yopanda cirema.
24 Ndipo ubwere nazo kwa Yehova, ndi ansembe athirepo mcere, ndi kuzipereka nsembe yopsereza ya Yehova.
25 Masiku asanu ndi awiri uzikonzera mbuzi tsiku ndi tsiku, ikhale nsembe yaucimo; akonzerenso mwana wa ng'ombe, ndi nkhosa yamphongo ya zoweta zopanda cirema.