8 ndi kuika ciundo cao pafupi pa ciundo canga, ndi mphuthu yao pa mbali ya mphuthu yanga, ndipo panali khoma lokha pakati pa iwo ndi Ine, nadetsa dzina langa loyera ndi zonyansa zao anazicita; cifukwa cace ndinawatha mu mkwiyo wanga.
9 Ataye tsono cigololo cao ndi mitembo ya mafumu ao kutali kwa Ine, ndipo ndidzakhala pakati pao kosatha.
10 Wabadwa ndi munthu iwe, onetsa nyumba ya Israyeli kacisiyu, kuti acite manyazi ndi mphulupulu zao; ndipo ayese muyeso wace.
11 Ndipo ngati akacita manyazi nazo zonse anazicita, uwadziwitse maonekedwe a kacisiyu, ndi muyeso wace, ndi poturukira pace, ndi polowera pace, ndi malongosoledwe ace onse, ndi malemba ace onse, ngakhale maonekedwe ace onse, ndi malamulo ace onse; nuwalembere pamaso pao, kuti asunge maonekedwe ace onse, ndi malemba ace onse, nawacite.
12 Lamulo la kacisi ndi ili: pamwamba pa phiri malire ace onse pozungulira pace azikhala opatulikitsa. Taonani, limeneli ndi lamulo la kacisi.
13 Ndipo miyeso ya guwa la nsembe, kuyesa mikono ndi iyi: (mkonowo ndiwo mkono ndi cikhato), tsinde lace likhale mkono, ndi kupingasa kwace mkono, ndi mkuzi wace m'mphepete mwace pozungulira pace kuyesa zala; ili ndi tsinde la guwali.
14 Ndi kuyambira kunsi kwace kunthaka, kufikira phaka lamunsi, mikono iwiri; ndi kupingasa kwace mkono umodzi; ndi kuyambira phaka laling'ono kufikira phaka lalikuru mikono inai; ndi kupingasa kwace mkono.