22 Kungakhale kutenga amasiye kapena osudzulidwa akhale akazi ao, asacite; koma atenge anamwali a mbeu ya nyumba ya Israyeli, kapena wamasiye ndiye wamasiye wa wansembe.
23 Ndipo aziphunzitsa anthu anga asiyanitse pakati pa zopatulika ndi zinthu wamba, ndi kuwazindikiritsa pakati pa zodetsa ndi zoyera.
24 Ndipo pakakhala mlandu, aimeko kuweruza; auweruze monga mwa maweruzo anga, ndipo azisunga malamulo anga, ndi malemba anga, pa madyerero anga onse oikika; napatulikitse masabata anga.
25 Ndipo asayandikire kwa munthu ali yense wakufa, angadzidetse; koma cifukwa ca atate, kapena mai, kapena mwana wamwamuna, kapena mwana wamkazi, kapena mbale, kapena mlongo wopanda mwamuna, nkuloleka kudzidetsa.
26 Ndipo atayeretsedwa amwerengere masiku asanu ndi awiri.
27 Ndipo tsiku loti alowa m'malo opatulika, bwalo lam'kati, kutumikira m'malo opatulika, apereke nsembe yace yaucimo, ati Ambuye Yehova.
28 Ndipo adzakhala naco colowa; Ine ndine colowa cao; musawapatsa colandira cao m'Israyeli; Ine ndine colandira cao.