19 Pamenepo anapita ndi ine podzera paja pali ku mbali ya cipata kumka ku zipinda zopatulika za ansembe zoloza kumpoto; ndipo taonani, kunali malo cauko kumadzulo.
20 Ndipo anati kwa ine, Pano ndipo ansembe aziphikira nsembe yoparamula, ndi nsembe yaucimo; kumenenso azioca mikate ya ufa wa nsembe, kuti asaturuke nazo ku bwalo lakunja ndi kupatulikitsa anthu,
21 Pamenepo anaturukira nane ku bwalo lakunja, nandipititsa ku ngondya zinai za bwaloli; ndipo taonani, m'ngondya monse munali bwalo.
22 M'ngondya zinai za bwalo munali mabwalo ocingika, m'litali mwace mikono makumi anai, kupingasa kwace makumi atatu; awa anai m'ngondyazi analingana muyeso wace.
23 Ndipo panali maguwa pozungulira pace m'menemo, pozungulira pace pa mabwalo anai; ndipo anamanga maguwawo ndi mafuwa pansi pace pozungulirapo.
24 Ndipo anati kwa ine, Izi ndi nyumba zophikiramo, kumene atumiki a kacisi aziphikira nsembe ya anthu.