11 Cidzakhala ca ansembe opatulidwa a ana a Zadoki, amene anasunga udikiro wanga osasokera, muja anasokera ana a Israyeli, ndi muja anasokera Alevi.
12 Ndi ciperekoco cikhale cao cotapa pa copereka ca dziko, ndico copatulikitsa pa malire a Alevi.
13 Ndipo polingana ndi malire a ansembe Alevi akhale nalo gawo la zikwi makumi awiri mphambu zisanu m'litali mwace, ndi zikwi khumi kupingasa kwace; m'litali mwace monse ndimo zikwi makumi awiri mphambu zisanu, ndi kupingasa kwace zikwi khumi.
14 Ndipo asagulitseko, kapena kulisintha, kapena kupitiriza zipatso zoyamba za dziko; pakuti liri lopatulika la Yehova.
15 Ndipo zikwi zisanu zotsalazo m'kupingasa kwace, cakuno ca zikwi makumi awiri mphambu zisanu, zikhale za nchito wamba za mudzi, za kumangapo zapabusa; ndi mudzi ukhale pakati pace.
16 Ndi miyeso yace ndi iyi: mbali ya kumpoto, mabango zikwi zinai mphambu mazana asanu; ndi mbali ya kumwela, zikwi zinai mphambu mazana asanu; ndi mbali ya kummawa, zikwi zinai mphambu mazana asanu; ndi mbali ya kumadzulo, zikwi zinai mphambu mazana asanu.
17 Ndipo mudziwo ukhale ndi busa lace; kumpoto mabango mazana awiri mphambu makumi asanu, kumwela mazana awiri mphambu makumi asanu, ndi kum'mawa mazana awiri mphambu makumi asanu, ndi kumadzulo mazana awiri mphambu makumi asanu.