3 Ndipo Rakele anati, Taonani mdzakazi wanga Biliha, mulowe kwa iye; ndipo iye adzabala pa maondo anga, kuti inenso ndionerepo ana pa iye.
4 Ndipo Rakele anampatsa iye Biliha mdzakazi wace akhale mkazi wace; ndipo Yakobo analowa kwa iye.
5 Ndipo Biliha anatenga pakati, nambalira Yakobo mwana wamwamuna.
6 Rakele ndipo anati, Mulungu wandiweruzira ine, namva mau anga, nandipatsa ine mwana; cifukwa cace anamucha dzina lace Dani.
7 Ndipo Biliha mdzakazi wace wa Rakele anatenganso pakati, nambalira Yakobo mwana wamwamuna waciwiri.
8 Ndipo Rakele anati, Ndi malimbano a Mulungu ndalimbana naye mkuru wanga, ndipo ndapambana naye; ndipo anamucha dzina lace Nafitali.
9 Pamene Leya anaona kuti analeka kubala, anatenga Zilipa mdzakazi wace, nampatsa iye kwa Yakobo kuti akhale mkazi wace.