1 Ndipo Mulungu anadalitsa Nowa ndi ana ace, nati kwa iwo, Mubalane, mucuruke, mudzaze dziko lapansi.
2 Kuopsya kwanu, ndi kucititsa mantha kwanu kudzakhala pa zinyama zonse za dziko lapansi, ndi pa zouluka zonse za m'mlengalenga; ndi pa zonse zokwawa pansi, ndi pa nsomba zonse za m'nyanja, zapatsidwa m'dzanja lanu.
3 Zoyenda zonse zamoyo zidzakhala zakudya zanu; monga therere laliwisi ndakupatsani inu zonsezo.
4 Koma nyama, m'mene muli moyo wace, ndiwo mwazi wace, musadye.
5 Zoonatu mwazi wanu wa miyoyo yanu ndidzafuna; pa dzanja la zinyama zonse ndidzaufuna: ndi pa dzanja la munthu, pa dzanja la mbale wace wa munthu ndidzaufuna moyo wa munthu.
6 Amene akhetsa mwazi wa munthu, ndi munthunso mwazi wace udzakhetsedwa: cifukwa m'cifanizo ca Mulungu Iye anampanga munthu.