3 Anamdzeranso masiku a Yehoyakimu mwana wace wa Yosiya, mfumu ya Yuda, kufikira Zedekiya mwana wace wa Yosiya mfumu ya Yuda atatsiriza zaka khumi ndi cimodzi; kufikira a ku Yerusalemu anatengedwa ndende mwezi wacisanu.
4 Ndipo anadza kwa ine mau a Yehova, kuti,
5 Ndisanakulenge iwe m'mimba ndinakudziwa, ndipo usanabadwe ndinakupatula iwe; ndinakuika kuti ukhale mneneri wa mitundu ya anthu.
6 Ndipo ndinati, Ha, Ambuye Mulungu! taonani, sindithai kunena pakuti ndiri mwana.
7 Koma Yehova anati kwa ine, Usati, ndine mwana pakuti udzanka kwa yense amene ndidzakutumako iwe, nudzanena conse cimene ndidzakuuza.
8 Usaope nkhope zao; cifukwa Ine ndiri ndi iwe kuti ndikulanditse iwe, ati Yehova.
9 Ndipo Yehova anaturutsa dzanja lace, na'khudza pakamwa panga; nati Yehova kwa ine, Taona ndaika mau anga m'kamwa mwako;