6 Cifukwa palibe akunga Inu, Yehova; muli wamkuru, ndipo dzina lanu liri lalikuru ndi lamphamvu,
7 Wosaopa Inu ndani, Mfumu ya amitundu? pakuti kukuopani ndi kwanu; pakuti mwa anzeru onse a amitundu, ndi m'maufumu ao onse, mulibe akunga Inu.
8 Koma onse pamodzi apulukira ndi kupusa; mtengo ndiwo cilangizo, copanda pace.
9 Abwera ndi siliva wa ku Tarisi, wosulasula wopyapyala ndi golidi wa ku Ufazi, nchito ya mmisiri ndi manja a woyenga; zobvala zao ndi nsaru ya madzi ndi yofiirira; zonsezi ndi nci ito za muomba.
10 Koma Yehova ndiye Mulungu woona; ndiye Mulungu wamoyo, mfumu yamuyaya; pa mkwiyo wace dziko lapansi lidzanthunthumira, ndi amitundu sangapirire ukali wace.
11 Muzitero nao, milungu imene sinalenga miyamba ndi dziko lapansi, iyo idzatha ku dziko lapansi, ndi pansi pa miyambayo.
12 Iye analenga dziko lapansi ndi mphamvu yace, nakhazikitsa dziko lapansi ndi nzeru yace, nayala thambo ndi kuzindikira kwace;