1 Wolungama ndinu, Yehova, pamene nditsutsana nanu mlandu; pokhapo ndinenane nanu za maweruzo; cifukwa canji ipindula njira ya oipa? cifukwa canji akhala bwino onyengetsa?
2 Inu mwabzyala iwo, inde, anagwiritsatu mizu; amera, inde, abalatu zipatso; muli pafupi m'kamwa mwao, muli patari ndi imso zao.
3 Koma inu, Yehova, mundidziwa ine; mundiona ine, muyesa mtima wanga ngati utani nanu; muwaturutse iwo monga nkhosa za kuphedwa, ndi kuwakonzeratu tsiku lakuphedwa.
4 Dziko lidzalira masiku angati, nilifota therere la minda yonse? cifukwa ca zoipa za iwo okhalamo, zithedwa zinyama, ndi mbalame; pakuti iwo anati, Iye sadzaona citsiriziro cathu.