3 Akuru ao atuma ang'ono ao kumadzi; afika kumaenje, osapeza madzi; abwera ndi mitsuko yao yopanda kanthu; ali ndi manyazi, athedwa nzeru, apfunda mitu yao.
4 Cifukwa ca nthaka yocita ming'aru, pakuti panalibe mvula padziko, olima ali ndi manyazi, apfunda mitu yao.
5 Inde, nswalanso ya m'thengo ibala nisiya ana ace, cifukwa mulibe maudzu.
6 Mbidzi zinaima pamapiri oti se, zipumira mphepo wefuwefu ngati ankhandwe; maso ao alema, cifukwa palibe maudzu.
7 Zingakhale zoipa zathu zititsutsa ife, citani Inu cifukwa ca dzina lanu, Yehova; pakuti zobwerera zathu zacuruka; takucimwirani Inu.
8 Inu, ciyembekezo ca Israyeli, mpulumutsi wace nthawi ya msauko, bwanji mukhala ngati mlendo m'dziko, ngati woyendayenda amene apatuka usiku?
9 Bwanji mukhala ngati munthu wodabwa, ngati munthu wamphamvu wosatha kupulumutsa? koma Inu, Yehova, muli pakati pathu, tichedwa ndi dzina lanu; musatisiye.