1 Ndipo Yehova anati kwa ine, Ngakhale Mose ndi Samueli akadaima pamaso panga, koma mtima wanga sukadasamalira anthu awa; muwacotse iwo pamaso panga, aturuke.
2 Ndipo padzakhala, pamene adzati kwa iwe, Titurukire kuti? pamenepo uziti, Atero Yehova: Amene a kuimfa, anke kuimfa; amene a kulupanga, anke kulupanga; amene a kunjala, anke kunjala; ndi amene a kunsinga, anke kunsinga.
3 Ndipo ndidzaika pa iwo mitundu inai, ati Yehova, lupanga lakupha, agaru akung'amba, mbalame za m'mlengalenga, ndi zirombo zapansi, zakulusa ndi kuononga.
4 Ndipo ndidzawapereka akhale oopsetsa m'maufumu onse a dziko lapansi, cifukwa ca Manase mwana wa Hezekiya mfumu ya Yuda, cifukwa ca zija anacita m'Yerusalemu.
5 Pakuti ndani adzakucitira iwe cisoni, Yerusalemu? ndani adzakulirira iwe? ndani adzapatukira kudzafunsa za mkhalidwe wako?
6 Iwe wandikana Ine, ati Yehova, wabwerera m'mbuyo; cifukwa cace ndatambasulira dzanja langa pa iwe, ndi kukuononga iwe; ndatopa ndi kulekerera.