12 Koma iwo ati, Palibe ciyembekezero; pakuti ife tidzatsata zilingaliro zathu, ndipo tidzacita yense monga mwa kuuma kwa mtima wacewoipa.
13 Cifukwa cace atero Yehova; Funsanitu m'mitundu, ndani wamva zotero; namwali wa Israyeli wacita cinthu coopsetsa kwambiri.
14 Kodi matalala a Lebano adzalephera pa mwala wa m'munda? kodi adzaphwa madzi ozizira otsika kutari?
15 Pakun anthu anga andiiwala Ine, afukizira zopanda pace; apunthwitsa iwo m'njira zao, m'njira zakale kuti ayende m'njira za m'mbali, m'njira yosatundumuka;
16 kuti aliyese dziko lao likhale lodabwitsa, ndi: kutsonya citsonyere; yense wakupitapo adzadabwa, ndi kupukusa mutu wace.
17 Ndidzamwazamwaza iwo monga ndi mphepo ya kum'mawa pamaso pa adani; ndidzayang'anira pamsana pao, si nkhope yao, tsiku la tsoka lao.
18 Ndipo iwo anati, Tiyeni, tilingalire Yeremiya comcitira coipa; pakuti cilamulo sicidzathera wansembe, kapena uphungu wanzeru, kapena mau mneneri. Tiyeni, timpande iye ndi lilime, tisamvere iye mau ace ali onse.