6 Nyumba ya Israyeli inu, kodi sindingathe kucita ndi inu monga woumba uyu? ati Yehova. Taonani, monga dothi m'dzanja la woumba, momwemo inu m'dzanja langa, nyumba ya Israyeli.
7 Mphindi imene ndidzanena za mtundu wa anthu, kapena za ufumu, kuti ndizule ndi kupasula ndi kuononga;
8 ngati mtundu umene, ndaunenera, udzatembenuka kuleka coipa cao, ndidzaleka coipaco ndidati ndiwacitire.
9 Ndipo mphindi imene ndikanenera mtundu, ndi ufumu, kuti ndimangitse mudzi wace ndi kuuoka;
10 koma ukacita coipa pamaso panga, osamvera mau anga, pamenepo ndidzaleka cabwinoco, ndidati ndiwacitire.
11 Tsopano nenatu kwa anthu a Yuda, ndi kwa okhala m'Yerusalemu, kuti, Atero Yehova: Taonani, Ine ndipangira inu coipa, ndilingalira inu kanthu kakucitira inu coipa; mubwerere tsono inu nonse, yense ku njira yace yoipa, nimukonze njira zanu ndi macitidwe anu.
12 Koma iwo ati, Palibe ciyembekezero; pakuti ife tidzatsata zilingaliro zathu, ndipo tidzacita yense monga mwa kuuma kwa mtima wacewoipa.