1 Atero Yehova, Pita, nugule nsupa ya woumba, nutenge akuru a anthu, ndi akuru a ansembe;
2 nuturukire ku cigwa ca mwana wace wa Hinomu, cimene ciri pa khomo la cipata ca mapale, nulalikire kumeneko mau amene ndidzakuuza iwe;
3 nuti, Tamvani mau a Yehova, inu mafumu a Yuda, ndi okhala m'Yerusalemu; Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli atero, Taonani, ndidzatengera malo ano coipa, cimene ali yense adzacimva, makutu ace adzacita woo.
4 Cifukwa andisiya Ine, nayesa malo ano acilendo, nafukizira m'menemo milungu yina, imene sanaidziwa, iwowa, ndi makolo ao ndi mafumu a Yuda: nadzaza malo ano ndi mwazi wa osacimwa;