13 Muyimbire Yehova, mulemekeze Yehova; pakuti walanditsa moyo wa aumphawi m'dzanja la ocita zoipa.
14 Litembereredwe tsiku limene ndinabadwa; lisadalitsike tsiku limene amai wanga anandibala ine.
15 Atembereredwe munthu amene anatengera mau kwa atate wanga, kuti, Mwana wamwamuna anakubadwira iwe; ndi kumsekeretsatu iye.
16 Munthuyo akhale ngati midzi imene Yehova anapasula, osalekerera; amve mpfuu mamawa, ndi mkuwo pausana;
17 cifukwa sanandipha ine m'mimba; kuti mai wanga akhale manda anga, ndi mimba yace yaikuru nthawi zonse.
18 Cifukwa canji ndinaturuka m'mimba kuti ndione kutopa ndi kulira, kuti masiku anga athe ndi manyazi?