1 Yehova atero: Tsikira ku nyumba ya mfumu ya Yuda, ndi kunena komweko mau awa,
2 ndi kuti, Tamvani mau a Yehova, Inu mfumu ya Yuda, amene mukhala pa mpando wa Davide, inu, ndi atumiki anu, ndi anthu anu amene alowa pa zipata izi.
3 Yehova atero: Citani ciweruzo ndi cilungamo, landitsani ofunkhidwa m'dzanja la wosautsa; musacite coipa, musamcitire mlendo ciwawa, kapena ana amasiye, kapena akazi amasiye, musakhetse mwazi wosacimwa pamalo pano.
4 Pakuti ngati mudzacitadi ici pamenepo, padzalowa pa zipata za nyumba iyi mafumu okhala pa mpando wacifumu wa Davide, okwera m'magareta ndi pa akavalo, iye, ndi atumiki ace, ndi anthu ace.
5 Koma ngati simudzamva mau amenewa, Ine ndilumbira, pali Ine mwini, ati Yehova, nyumba iyi idzakhala yabwinja.
6 Pakuti Yehova atero za nyumba ya mfumu ya Yuda: Ndikuyesa iwe Gileadi, ndi mutu wa Lebano; koma ndidzakuyesa iwe cipululu, ndi midzi yosakhalamo anthu.
7 Ndipo ndidzakupangiratu iwe opasula, yense ndi zida zace; ndipo adzadula mikungudza yako yosankhika nadzaiponya m'moto.