14 Ndipo ndidzapezedwa ndi inu, ati Yehova, ndidzabwezanso undende wanu, ndipo ndidzasonkhanitsa inu kwa mitundu yonse, ndi kumalo konse kumene ndinakupitikitsirani inu, ati Yehova; ndipo ndidzakubwezeraninso kumalo kumene ndinakutengani inu andende.
15 Pakuti mwati, Yehova watiutsira ife aneneri m'Babulo.
16 Pakuti Yehova atero za mfumu imene ikhala pa mpando wacifumu wa Davide, ndi za anthu onse amene akhala m'mudzi uno, abale anu amene sanaturukira pamodzi ndiinu kundende;
17 Yehova wa makamu atero: Taonani, ndidzatuma pa iwo lupanga, ndi njala, ndi caola, ndipo ndidzayesa iwo onga nkhuyu zoola, zosadyeka, pokhala nzoipa.
18 Ndipo ndidzatsata iwe ndi lupanga, ndi njala, ndi caola, ndipo ndidzawapereka akhale oopsyetsa m'maufumu onse a dziko la pansi, akhale citemberero, ndi codabwitsa, ndi cotsonyetsa, ndi citonzo, kwa mitundu yonse kumene ndinawapitikitsirako;
19 cifukwa sanamvera mau anga, ati Yehova, amene ndinawatumizira ndi atumiki anga aneneri, ndi kuuka mamawa ndi kuwatuma, koma munakana kumva, ati Yehova.
20 Pamenepo tamvani inu mau a Yehova, inu nonse a m'ndende, amene ndacotsa m'Yerusalemu kunka ku Babulo.