1 Mau amene anadza kwa Yeremiya kucokera kwa Yehova, kuti,
2 Atero Yehova, Mulungu wa Israyeli, kuti, Lemba m'buku mau onse amene ndanena kwa iwe.
3 Pakuti, taona, masiku adzadza, ati Yehova, amene ndidzabwezanso undende wa anthu anga Aisrayeli ndi Ayuda, ati Yehova; ndipo ndidzawabwezera ku dziko limene ndinapatsa makolo ao. Ndipo adzakhala nalo.
4 Awa ndi mau ananena Yehova za Israyeli ndi Yuda.
5 Pakuti Yehova atero: Tamva ife mau akunthunthumira, ndi amantha, si amtendere.
6 Funsani tsopano, ndi kuona ngati mwamuna aona mwana; cifukwa canji ndiona mwamuna ndi manja ace pa cuuno cace, monga mkazi alinkubala, ndi nkhope zao zotumbuluka?