4 ndipo Zedekiya mfumu ya Yuda sadzapulumuka m'dzanja la Akasidi, koma adzaperekedwadi m'dzanja la mfumu ya Babulo, ndipo adzanena ndi iye pakamwa ndi pakamwa, ndipo adzaonana maso ndi maso;
5 ndipo adzatsogolera Zedekiya kunka ku Babulo, ndipo adzakhala komwe kufikira ndidzamzonda, ati Yehova: ngakhale mudzamenyana ndi Akasidi, simudzapindula konse?
6 Ndipo Yeremiya anati, Mau a Yehova anadza kwa ine, kuti,
7 Taonani, Hanameli mwana wa Salumu mbale wa atate wako adzadza kwa iwe, kuti, Ugule munda wanga uli ku Anatoti; pakuti mphamvu yakuombola ndi yako kuugula.
8 Ndipo Hanameli mwana wa mbale wa atate wanga anadza kwa ine m'bwalo la kaidi monga mwa mau a Yehova, nati kwa ine, Gulatu munda wanga, wa ku Anatoti, m'dziko la Benjamini; pakuti mphamvu yakulowa ndi yakuombola ndi yako; udzigulire wekha. Pamenepo ndinadziwa kuti awa ndi mau a Yehova.
9 Ndipo ndinagula mundawo wa ku Anatoti kwa Hanameli mwana wa cibale wa atate wanga, ndimyesera ndalama, masekele khumi ndi asanu ndi awiri a siliva.
10 Ndipo ndinalemba cikalataco, ndicisindikiza, ndiitana mboni zambiri, ndiyesa ndalama m'miyeso.