5 Adza kumenyana ndi Akasidi, koma adzangozidzaza ndi mitembo ya anthu, amene ndawapha m'mkwiyo wanga ndi mu ukali wanga, amene ndabisira mudzi uno nkhope yanga cifukwa ca zoipa zao zonse.
6 Taonani, ndidzautengera moyo ndi kuuciritsa, ndi kuwaciritsa; ndipo ndidzawaululira iwo kucuruka kwa mtendere ndi zoona.
7 Ndipo ndidzabweza undende wa Yuda ndi wa Israyeli, ndipo ndidzamangitsa mudzi wao, monga poyamba paja,
8 Ndipo ndidzawayeretsa kucotsa mphulupulu yao, imene anandicimwira Ine; ndipo ndidzakhululukira mphulupulu zao zimene anandicimwira, nandilakwira Ine.
9 Ndipo ndidzayesa mudzi uno cifukwa ca kukondwa, ndi ciyamiko ndi ulemerero, pamaso pa amitundu onse a pa dziko lapansi, amene adzamva zabwino zonse ndidzawacitirazo, ndipo adzaopa nadzanthunthumira cifukwa ca zabwino zonse ndi mtendere wonse zimene ndidzaucitira.
10 Atero Yehova: M'malo muno, m'mene muti, Ndi bwinja, mopanda munthu, mopanda nyama, m'midzi ya Yuda, m'makwalala a Yerusalemu, amene ali bwinja, opanda munthu, opanda wokhalamo, opanda nyama,
11 mudzamvekanso mau akukondwa ndi mau akusekera, mau a mkwati ndi mau a mkwatibwi, mau a iwo akuti, Myamikireni Yehova wa makamu, pakuti Yehova ndiye wabwino, cifundo cace ncosatha; ndi a iwo akutengera nsembe zoyamikira m'nyumba ya Yehova. Pakuti ndidzabweza undende wa dziko monga poyamba, ati Yehova.