1 Ndipo panali mwezi wacisanu ndi ciwiri, Ismayeli mwana wa Netaniya, mwana wa Elisama, wa mbeu ya mfumu, ndi kapitao wamkuru wa mfumu, ndi anthu khumi pamodzi ndi iye, anadza kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu ku Mizipa; pamenepo anadya pamodzi m'Mizipa.
2 Ndipo anauka Ismayeli mwana wa Netaniya, ndi anthu khumi okhala naye, namkantha Gedaliya mwana wa Ahikamu mwana wa Safani ndi lupanga, namupha iye, amene mfumu ya ku Babulo inamuika wolamulira dziko.
3 Ismayeli naphanso Ayuda onse okhala naye Gedaliya pa Mizipa, ndi Akasidi amene anakomana nao komweko, amuna a nkhondo.
4 Ndipo panali atapita masiku awiri atamupha Gedaliya, anthu osadziwa,
5 anadza anthu ocokera ku Sekemu, ndi ku Silo, ndi ku Samariya, anthu makumi asanu ndi atatu, atameta ndebvu zao, atang'amba zobvala zao, atadzitematema, ana tenga nsembe zaufa ndi zonunkhira m'manja mwao, kunka nazo ku nyumba ya Yehova.