Yeremiya 44:22-28 BL92

22 ndipo Yehova sanatha kupirirabe, cifukwa ca macitidwe anu oipa, ndi cifukwa ca zonyansa zimene munazicita; cifukwa cace dziko lanu likhala bwinja, ndi cizizwitso, ndi citemberero, lopanda wokhalamo, monga lero lomwe.

23 Cifukwa mwafukiza, ndi cifukwa mwacimwira Yehova, osamvera mau a Yehova, osayenda m'cilamulo cace, ndi m'malemba ace, ndi m'mboni zace, cifukwa cace coipaci cakugwerani, monga lero lomwe.

24 Ndiponso Yeremiya anati kwa anthu onse, ndi kwa akazi onse, Tamvani mau a Yehova, nonse Ayuda amene muli m'dziko la Aigupto.

25 Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli, Inu ndi akazi anu mwanena ndi m'kamwa mwanu, ndi kukwaniritsa ndi manja anu kuti, Tidzacita ndithu zowinda zathu taziwindira, kufukizira mfumu yaikazi ya kumwamba, ndi kumthirira iye nsembe zothira; khazikitsanitu zowinda zanu, citani zowinda zanu.

26 Cifukwa cace tamvani mau a Yehova, nonse Ayuda okhala m'dziko la Aigupto: Taonani, ndalumbira, Pali dzina langa lalikuru, ati Yehova, kuti dzina langa silidzachulidwanso m'kamwa mwa munthu ali yense wa Yuda m'dziko la Aigupto, ndi kuti, Pali Yehova Mulungu.

27 Taonani, ndiwayang'anira kuwacitira zoipa, si zabwino; ndipo amuna onse a Yuda okhala m'dziko la Aigupto adzathedwa ndi lupanga ndi njala, mpaka kutha kwao.

28 Ndipo iwo amene adzapulumuka kulupanga adzabwera kuturuka ku dziko la Aigupto kulowa m'dziko la Yuda, owerengeka; ndipo otsala onse a Yuda, amene analowa m'dziko la Aigupto kuti akhale m'menemo, adzadziwa ngati adzatsimikizidwa mau a yani, kapena anga, kapena ao.