28 Inu okhala m'Moabu, siyani midzi, khalani m'thanthwe; nimukhale monga njiwa imene isanja cisanja cace pambali pakamwa pa dzenje.
29 Ife tamva kudzikuza kwa Moabu, wadzikuza ndithu, kunyang'wa kwace, ndi kunyada kwace, ndi kudzitama kwace, ndi kudzikuza kwa mtima wace.
30 Ine ndidziwa mkwiyo wace, ati Yehova, kuti uli cabe; zonyenga zace sizinacita kanthu.
31 Cifukwa cace ndidzakuwira Moabu; inde, ndidzapfuulira Moabu yense, adzalirira anthu a ku Kirere.
32 Iwe mpesa wa Sibima; ndidzakulirira iwe ndi kulira kopambana kulira kwa Yazeri, nthambi zako zinapitirira nyanja, zinafikira ku nyanja ya Yazeri; wakufunkha wagwera zipatso zako za mpakasa ndi mphesa zako.
33 Ndipo kusekera ndi kukondwa kwacotsedwa, ku munda wobala ndi ku dziko la Moabu; ndipo ndaletsa vinyo pa zoponderamo; sadzaponda ndi kupfuula; kupfuula sikudzakhala kupfuula.
34 Kuyambira kupfuula kwa Hesiboni mpaka ku Eleale, mpaka ku Yahazi anakweza mau, kuyambira pa Zoari mpaka ku Horonaimu, ku Egilati-Selisiya; pakuti pa madzi a ku Nimurimu komwe padzakhala mabwinja.