3 Wauta asakoke uta wace, asadzikweze m'malaya ace acitsulo; musasiye anyamata ace; muononge ndithu khamu lace lonse.
4 Ndipo adzagwa ophedwa m'dziko la Akasidi, opyozedwa m'miseu yace.
5 Pakuti Israyeli ndi Yuda sasiyidwa ndi Mulungu wao, ndiye Yehova wa makamu: ngakhale dziko lao ladzala ndi ucimo kucimwira Woyera wa Israyeli.
6 Thawani pakati pa Babulo, yense apulumuke moyo wace; musathedwe m'coipa cace; pakuti ndi nthawi ya kubwezera cilango; Yehova adzambwezera iye mphotho yace.
7 Babulo wakhala cikho cagolidi m'dzanja la Yehova, amene analedzeretsa dziko lonse lapansi; amitundu amwa vinyo wace; cifukwa cace amitundu ali ndi misala.
8 Babulo wagwa dzidzidzi naonongedwa; mumkuwire iye; mutengere zowawa zace bvunguti, kapena angacire.
9 Tikadaciritsa Babulo koma sanacire; mumsiye iye, tipite tonse yense ku dziko lace; pakuti ciweruziro cace cifikira kumwamba, cinyamulidwa mpaka kuthambo,