52 Cifukwa cace, taona, masiku alinkudza, ati Yehova, amene ndidzaweruza mafano ace; ndipo pa dziko lace lonse olasidwa adzabuula.
53 Ngakhale Babulo adzakwera kumwamba, ngakhale adzalimbitsa msanje wa mphamvu yace, koma kucokera kwa Ine akufunkha adzafika kwa iye, ati Yehova.
54 Mau akupfuula ocokera ku Babulo, ndi a cionongeko cacikuru ku dziko la Akasidi!
55 pakuti Yehova afunkha Babulo, aononga m'menemo mau akuru; ndipo mafunde ace adzakokoma ngati madzi ambiri, mau ao aphokosera;
56 pakuti wakufunkha wafika kwa iye, kwa Babulo, ndi anthu ace olimba agwidwa, mauta ao atyokatyoka, pakuti Yehova ndiye Mulungu wakubwezera, adzabwezera ndithu.
57 Ndipo ndidzaledzeretsa akuru ace ndi anzeru ace, akazembe ace ndi ziwanga zace, ndi anthu ace olimba; ndipo adzagona cigonere, sadzanyamuka, ati Mfumu, dzina lace ndi Yehova wa makamu.
58 Yehova wa makamu atero: Makoma otakata a Babulo adzagwetsedwa ndithu, ndi zitseko zace zazitari zidzatenthedwa ndi moto; anthu adzagwirira nchito cabe, ndi mitundu ya anthu idzagwirira moto, nidzatopa.