56 pakuti wakufunkha wafika kwa iye, kwa Babulo, ndi anthu ace olimba agwidwa, mauta ao atyokatyoka, pakuti Yehova ndiye Mulungu wakubwezera, adzabwezera ndithu.
57 Ndipo ndidzaledzeretsa akuru ace ndi anzeru ace, akazembe ace ndi ziwanga zace, ndi anthu ace olimba; ndipo adzagona cigonere, sadzanyamuka, ati Mfumu, dzina lace ndi Yehova wa makamu.
58 Yehova wa makamu atero: Makoma otakata a Babulo adzagwetsedwa ndithu, ndi zitseko zace zazitari zidzatenthedwa ndi moto; anthu adzagwirira nchito cabe, ndi mitundu ya anthu idzagwirira moto, nidzatopa.
59 Mau amene Yeremiya mneneri anauza Seraya mwana wa Neriya, mwana wa Maseya, pamene iye ananka ndi Zedekiya mfumu ya Yuda ku Babulo caka cacinai ca ufumu wace. Ndipo Seraya anali kapitao wa cigono cace.
60 Ndipo Yeremiya analemba m'buku coipa conse cimene cidzafika pa Babulo, mau onse awa olembedwa za Babulo.
61 Ndipo Yeremiya anati kwa Seraya, Pamene ufika ku Babulo, samalira kuti uwerenge mau awa onse,
62 nuti, inu Yehova, mwanena za malo ano, kuti mudzawatha, kuti asakhalemo, ngakhale anthu ngakhale nyama, koma akhale bwinja nthawi za nthawi.