23 Ndipo pambali pace panali makangaza makumi asanu ndi anai kudza asanu ndi limodzi; ndipo makangaza onse anali zana limodzi pamade pozungulira pace.
24 Ndipo kapitao wa alonda anatenga Seraya mkuru wansembe, ndi Zefaniya wansembe waciwiri, ndi akudikira pakhomo atatu;
25 ndipo m'mudzi anatenga kazembe amene anali woyang'anira anthu a nkhondo ndi amuna asanu ndi awiri a iwo akuona nkhope ya mfumu, amene anapezedwa m'mudzi; ndi mlembi wa kazembe wa nkhondo, amene akamemeza anthu a m'dziko; ndi amuna makumi asanu ndi limodzi a anthu a m'dziko, amene anapezedwa pakati pa mudzi.
26 Ndipo Nebuzaradani kapitao wa alonda anatenga iwo, nadza nao kwa mfumu ya ku Babulo ku Ribila.
27 Ndipo mfumu ya ku Babulo anawakantha, nawapha pa Ribila m'dziko la Hamati. Comweco Yuda anatengedwa ndende kuturuka m'dziko lace.
28 Amenewa ndi anthu amene Nebukadirezara anatenga ndende: caka cacisanu ndi ciwiri, Ayuda zikwi zitatu kudza makumi awiri ndi atatu;
29 caka cakhumi ndi cisanu ndi citatu ca Nebukadirezara iye anatenga ndende kucokera m'Yerusalemu anthu mazana asanu ndi atatu kudza makumi atatu ndi awiri;