11 Ndipo ndidzayesa Yerusalemu miyulu, mbuto ya ankhandwe; ndipo ndidzayesa midzi ya Yuda bwinja, lopanda wokhalamo.
12 Wanzeru ndani, kuti adziwe ici? ndani iye amene kamwa la Yehova lanena naye, kuti acilalikire? cifukwa cace dziko litha ndi kupserera monga cipululu, kuti anthu asapitemo?
13 Ndipo Yehova ati, Cifukwa asiya cilamulo canga ndinaciika pamaso pao, ndipo sanamvera mau anga, osayenda m'menemo;
14 koma anatsata kuuma kwa mtima wao, ndi Baala, monga makolo ao anawaphunzitsa;
15 cifukwa cace atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli, Taonani, ndidzadyetsa anthu awa civumulo, ndi kuwamwetsa madzi andulu.
16 Ndidzawabalalitsanso mwa amitundu, amene iwo kapena makolo ao sanawadziwa; ndipo ndidzatumiza lupanga, liwatsate mpaka ndawatha.
17 Atero Yehova wa makamu, Kumbukirani inu, ndi kuitana akazi akulira, adze; aitaneni akazi ocenjera, kuti adze;