14 Ndipo mau a Yehova anandidzera kuti,
15 Wobadwa ndi munthu iwe, abale ako, inde abale ako amuna a cibale cako, ndi nyumba yonse ya Israyeli, yonseyi ndiwo amene okhala m'Yerusalemu ananena nao, Muzikhala kutali kwa Yehova; dziko ili lapatsidwa kwa ife, likhale colowa cathu;
16 cifukwa cace uziti, Atero Yehova Mulungu, Ngakhale ndawacotsa kutali mwa amitundu, ngakhalenso ndawabalalikitsa m'maiko, koma ndidzawakhalira malo opatulika kanthawi ku maiko adafikako.
17 Cifukwa cace uziti, Atero Yehova Mulungu, Ndidzakumemezani ku mitundu ya anthu, ndi kukusonkhanitsani mucoke m'maiko m'mene munabalalikiramo, ndipo ndidzakuninkhani dziko la Israyeli.
18 Ndipo adzafikako, nadzacotsako zonyansa zace zonse, ndi zace zonse zakuipitsamo.
19 Ndipo ndidzawapatsa mtima umodzi, ndi kuika mzimu watsopano m'kati mwao; ndipo ndidzawacotsera mtima wamwala m'thupi mwao, ndi kuwapatsa mtima wamnofu;
20 kuti ayende m'malemba anga, ndi kusunga maweruzo anga, ndi kuwacita; ndipo adzakhala anthu anga, ndi Ine ndidzakhala Mulungu wao.