36 Monga ndinaweruza makolo anu m'cipululu ca dziko la Aigupto, momwemo ndidzaweruza inu, ati Ambuye Yehova.
37 Ndipo ndidzakupititsani pansi pa ndodo ya mbusa ndi kukulowetsani m'cimango ca cipangano;
38 ndipo ndidzasankhula mwa inu opanduka ndi ondilakwira, ndidzawaturutsa m'dziko logoneramo iwo; koma sadzalowa m'dziko la Israyeli; motero mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
39 Ndipo inu, nyumba ya Israyeli, atero Ambuye Yehova, mukani, tumikirani yense mafano ace, ndi m'tsogolo momwe, popeza simundimvera Ine; koma musaipsanso dzina langa lopatulika ndi zopereka zanu ndi mafano anu.
40 Pakuti pa phiri langa lopatulika, pa phiri lothubvuka la Israyeli, ati Ambuye Yehova, pomwepo onse a nyumba ya Israyeli, onsewo adzanditumikira Ine m'dzikomo; pomwepo ndidzawalandira, ndi pomwepo ndidzafuna nsembe zanu zokweza, ndi zoyamba za msonkho wanu, pamodzi ndi zopatulika zanu zonse.
41 Ngati pfungo lokoma ndidzakulandirani pakukuturutsani mwa mitundu ya anthu, ndipo ndidzakusonkhanitsani kukucotsani m'maiko munabalalikiramo, ndipo ndidzazindikirika Woyera mwa inu pamaso pa amitundu.
42 Ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pakukulowetsani Ine m'dzil ko la Israyeli, m'dzikoli ndinalikwezera dzanja langa kulipereka kwa makolo anu.